Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 41
Matigari
sidikira ngakhale mfumu!”
“Kodi unamvapo zokhudza anthu a m’banja langa
kufakitaleko?”
“Anthu a m’banja la Matigari?” anafunsa Ngaruro. “Kodi
inuyo mukuganiza kuti ifeyo tili m’banja la ndani?” ananena
mawu amenewa kwinaku akumweturira.
“Ukawauze anthu a m’banja langa kuti: ‘Mtsamunda
Williams tamutsogoza. Nayenso wantchito wake John Boy
tamutsira dothi m’nkhutu. Tsopano tiyeni tibwerere kunyumba,
tikayatse moto komanso tikamange nyumba yathu limodzi.’”
“Taimani kaye,” Ngaruro anatero, akuoneka kuti
wazindikira zinazake. “Williams? Boy? Mmodzi mwa mabwana
athu pafakitaleyi amadziwika ndi dzina loti Williams. Robert
Williams. Wachiwiri wake dzina lake ndi John Boy.”
“Osaiwalatu kuti dzina ndi moto,” Anatero Matigari.
“Zoona,” Ngaruro anayankha. “Uthenga mwandiuzawu
ndikafikitsa. Tikakakumana ndikawauza kuti: ‘Mtsamunda
Williams tamutsogoza. Nayenso wantchito wake John Boy
tamutsira dothi m’nkhutu.’ Ndikasonkhanitsa anthu onse a
m’banja mwanga n’kuwauza kuti: ‘Tsopano tiyeni tibwerere
kunyumba, tikayatse moto komanso tikamange nyumba yathu
limodzi.’ Anzeru akazindikira zimene ndikutanthauza.”
Ngaruro wa Kiriro anauyamba ndipo zinkangokhala ngati
Matigari wamupatsa mangolomera.
Matigari ndi Muriuki anamuperekeza ndi maso ndipo
anaonanso namtindi wa ogwira ntchito ukulowera kufakitale
kuja. Kenako Ngaruro analowa m’chigulu cha ogwira
ntchitowo ndipo sanaonekenso. Nthawi ya nkhomaliro inali
itangotsala pang’ono kutha. Ndipo anthu ambiri tsopano
40