Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 40
Matigari
Pamalowo panali bala yadenga la malata yomangidwa ndi
miyala, ndipo chakumapeto kwa balayi kunali malo ogulitsira
zakudya. Malowa anali omangidwa ndi matabwa ndipo denga
lake linali lofoleredwa ndi mapepala. Panalinso kampanda
komangidwa ndi makatoni ndiponso masaka.
Anthu ankatha kugula chakudya chawo n’kudyera malowa
kapena kukadyera mubala ija. Koma ambiri ankasankha
kukhala pomwepo ndipo munthu unkatha kuwaona
atatanganidwa ndi kujegweda chakudya chawo. Pepala la
mitengo ya zakudya zomwe zinkagulitsidwa pamalowa
linamatidwa pakhoma.
MATAHA HOTELO, BARA NDI RESITILANTI
Ugali wa Nyama Yowotcha ndi Supu; Nsima ya Masamba ndi
Nyemba; Nsima ndi Chipere; Tchana; Soya; Tiyi; Mkaka; Phala;
Chapate, Buledi, Samusa, Masikono ndi Zina
TIMAGULITSA CHILICHONSE KUPATULAPO CHIMENE
SIMUDYA
Ogwira ntchito kufakitale kuja anali atayamba kubwerera
tsopano. Anthuwa ankabwerera m’magulu a anthu atatu, anayi
komanso asanu.
“Ineyo ndisalowe koma,” anatero Ngaruro. “Tinagwirizana
kuti tipite mofulumira lero chifukwa kukakhala msonkhano wa
ogwira ntchito onse panja pafakitale. Tikufuna tichite sitiraka.”
“Mukufuna mupange sitiraka?” anafunsa Matigari.
“Inde, tiyamba kunyanyala ntchito 2 koloko masanawa . . .
Umumu mupeza chakudya chilichonse chomwe mungakonde
kudya. Mupemphe madzi kuti mupukute magazi ali kunkhope
kwanuwo. Ineyo ndithamange. Nthawi sikudikira ine, ndipo
39