Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 39

Matigari kenako ndinatulukira m’minda yanthochi. Ndinawoloka mitsinje, ndinakwera mapiri mpaka ndinakalowa m’nkhalango. Mtsamunda Williams ananditsatira ndipo panayambika nkhondo ya wafawafa kuti zioneke kuti wamphamvu anali ndani komanso kuti bwana m’chipetachi anali uti.” “Mmenemutu ndi mmene zinayambira kuti tilimbane kwa zaka zonsezi.” “Ndi dzulodzuloli pamene zaoneka kuti wamphamvu ndi ndani. Mtsamunda Williams wabwira dothi! Ndamuonetsa kiyama! Nditam’kantha, ndinamuzemberera n’kufika pamene anagwera kuti ndikatsimikizere kuti wafadi. Analidi atasiya gaga. Ndinamuponda pachifuwa n’kutenga mfuti yake n’kuilozetsa m’mwamba ndipo ndinayamba kuimba nyimbo yachipambano posangalala kuti ndagwetsa mdani wanga.” “Ndiye lero ndi limene ndatuluka m’nkhalango n’kubwera kuno. Ndikufuna ndisonkhanitsenso banja langa.” Pamene ankafotokoza zimenezi, maso ake ankawala ngati nthanda. Zimene ankanenazi zinamufika pamtima Muriuki komanso Ngaruro wa Kiriro moti sanazindikire zoti afika pamalo ogulitsira zakudya paja. Nkhaniyi inali itawaponyera patali, kale kwambiri pamene mauta ndi mivi ya adani inkagwedeza mitengo ndi mitsitsi yomwe, mwinanso ngakhale kutekesa mapiri. “Ndiye ndi angati amene atsala m’nkhalango kuti moto wa ufulu wathu usazime?” Ngaruro wa Kiriro anafunsa motero. “Limenelo sindiyakha, funsa lina?” “Chabwino, basi ndamvetsa. Tafika tsopano. Malo ogulitsira zakudya aja ndi amenewa.” 38