Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 38
Matigari
nyumba yake. Tuluka m’nyumba mwangamu msanga. Iwenso
manja uli nawo ako! Munthu wankhanza komanso wadyera
ngati iwe sindinamuonepo! Pita ukamange nyumba yako.
Ukapanda kutuluka m’nyumba yangayi uona mbonaona. Ndi
ndani anakunamiza kuti womanga alibe maso kuti awone, mutu
kuti aganize komanso lilime kuti ayankhule?’”
“Pamene ndinkamaliza kunena zimenezi n’kuti
ndikunjenjemera ngati mtengo mumphepo yankhuntho.
Sindinkanjenjemera chifukwa chozizidwa kapena chifukwa cha
mantha. Ndinkanjenjemera ndi nkwiyo. Ndinali ndi nkwiyo
womwe unabwera mamba a umbuli wa zaka zambiri
atathothoka m’maso mwanga. Tsopano ndinali nditayamba
kuganiza ngati munthu.”
“Nthawi yomweyo Mtsamunda Williams anagwira
thenifolo. Nane ndinathamangira pomwe ankasunga mfuti yake
ndipo ndinaitengadi. Ndinaitenga n’kuigwira m’manja. Kenako
ndinagwada ndi bondo limodzi nditamulozetsa mfutiyo. Koma
ndikukuuzani padzikoli sipadzaleka kuchitika zodabwitsa!
Simungakhulupirire zimene zinachitika. Ndi John Boy, munthu
wakuda ngati ine ndemwe, wantchito wa Mtsamunda Williams,
yemwe anamupulumutsa. Sindikumbukira bwinobwino kuti
anatulukira kuchokera kuti. Mwina ankachokera kukhitchini.
John Boy anandilumphira kumsana kwinaku akukuwa. Mfuti ija
inagwera pansi ndipo tinayamba kulimbana pamene paja.
Ndinkafunitsitsa nditatenganso mfutiyo. Koma Mtsamunda
Williams anabwera kudzamuthandiza John Boy. Ndiye
ndinaona kuti popanda mfuti , zinthu zindidera. Choncho
ndinakokera mphamvu, n’kutsomphoka m’manja mwa John
Boy. Kenako ndinalumpha n’kutulukira pazenera.
Ndinathawira m’minda ya tiyi, n’kulowa m’minda ya chimanga,
37