Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 37
Matigari
Koma ndikamati ndiyambe kusangalala kuti ndapambana,
ndinkamva zoti anthu ena amuona ali penapake,
akundifunafuna kuti andiphe. Nthawi zina zipolopolo zake
zinkandilowa m’nthupi. Ndinkakwawa, kuyenda motsimphina
n’kukabisala kuphanga mpaka bala langa litapola. Nthawi
zinanso ankangotsala pang’ono kundizimitsa. Mwamwayi
Mulungu ankakhala asanakonzeke kundilandira mu Ufumu
wake. Koma kodi mukudziwa kuti tinkalimbirana chiyani?”
“Nyumba. Nyumba yanga.”
“Mwaona, ndinamanga nyumba ndi manja anga. Koma
Mtsamunda Williams anayamba kugonamo ine n’kumagona
pakhonde. Ndinkalima minda yomwe inazungulira nyumba
yangayo, koma ndi Mtsamunda Williams amene ankakolola
mbewu zake. Iye ankangondisiya kuti ndizikunkha zotsala za
m’mundamo. Ndinkagwira ntchito yotopetsa m’mafakitale,
koma Mtsamunda Williams ankatolera ndalama zonse
n’kumakazivundika kubanki ndipo ineyo ankandiponyera
kakhobidi kuti ndikagulire m’gaiwa. Ndalama zonse zomwe
tinkapanga zinkatafunidwa ndi mtsamunda ameneyu.
Ndikuganiza kuti mukudziwa bwino mbiri imeneyi.
Ndinkalima mbewu ndi manja angawa, koma zokolola zonse
zinkatengedwa ndi Mtsamunda Williams. Dzikoli ndi lopanda
chilungamo ntheradi! Dziko limene telala amavala nsanza,
mlimi kumadya zotoleza, m’misiri womanga kumagona
pakhonde. Ndiye nditatopa nazo, tsiku lina ndinaganiza
zothana naye. Ndinamuuza kuti, ‘Mtsamunda Williams,
umakolola pomwe sunafese, tsopano imva kulira kwa mphalasa
komanso lipenga la chilungamo. Telala akufuna zovala zake.
Mlimi akufuna nthaka yake komanso zotsatira za thukuta lake
lomwe wakhala akukhetsa zaka zonsezi. Womanga akufuna
36