Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 36
Matigari
“Anthu amenewa ndi amene analowa m’thengo
kukamenyera ufulu wathu wodzilamulira.” Ngaruro anayankha
motero. “Anthu amanena kuti ena mwa anthu amenewa adakali
kunkhalango.”
“Chifukwa chiyani?”
“Akufuna kuti moto wa ufulu wathu usazime,” Ngaruro
anayankha.
“Chifukwa?”
“Sizingakhale bwino motowo utazima. Kodi ukudziwa kuti
moto wa ufulu wathu unayatsidwa m’nkhalango komanso
m’mapirimu zaka zambiri zapitazo?” Ngaruro anapitiriza
motero.
“Zoonadi,” anatero Matigari. “Anawa sangadziwedi nkhani
imeneyi, achepa nazo. Tangoganizani zimene zachitikira ineyo.
Ineyo ndi Mtsamunda Williams takhala tikulimbana kwa zaka
zambiri m’mapiri komanso m’nkhalango zimenezi.
Tinkasakanasakana m’mapanga, m’mitsinje, zigwa komanso
malo ena osiyanasiyana. Nthawi zina ndinkatha kumuona ali
chapatali, koma pamene ndinkati ndimulase nacho chipolopolo,
ndinkangozindikira wazimiririka m’tchire, kenako
sankaonekanso chifukwa cha mdima wa m’nkhalango.”
“Nthawi zina ankandipezeketsa. Koma akamafuna kuti
andiwombere ndinkakhala ndathawa. Ndinkagudubuka pansi,
kukwawa komanso kuyenda ngati njoka ndipo ankalephera
kundigwiranso. Zimenezi zinachitika kwa masiku, miyezi,
komanso zilumika zambirimbiri.”
“Palibe amene ankafuna kugonjera mnzake. Nthawi zina
ndinkamuombera n’kumaganiza kuti ndamutumiza ku Gehena.
35