Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 35
Matigari
“Usadandaule,” bambo uja anatero kwinaku akudzuka
mwamphamvu ngati wabwereranso ku unyamata. Anachita
zimenezi modzilimbitsa mtima ngakhale ankamva kupweteka.
Anatolanso zinthu zake zija, maso ake akuyang’ana ngati
akuone zomwe zidzachitike m’tsogolo.
“Tipitira limodzi kunyumba yanga. Ndikutengera
kunyumba yanga kuti ukaone zoti sikuti ndinangotaya nthawi
yanga pachabe pomenya nkhondo yolimbana ndi Mtsamunda
Williams . . .”
Ngaruro ndi Muriuki anayang’anizana modabwa atamva
mawu amenewa. Iwo ankadzifunsa kuti, “Kodi makwinya onse
anali pankhope pake aja alowera kuti?”
“Dzina lanu ndi ndani?” Anafunsa motero Ngaruro wa
Kiriro.
“Matigari ma Njiruungi.”
“Matigari ma Njiruungi?”
“Inde, dzina langa ndi limenelo.”
Anayenda molunji kumsika kuja ndipo aliyense
sankayankhula mnzake.
“Matigari ma Njiruungi,” Ngaruro anabwerezanso dzina
lija. “Anthu omwe anapulumuka nkhondo yomenyera ufulu
wathu.”*
*Matigari ma Njiruungi (Gikuyu): Tanthauzo lenileni la mawuwa ndi, “anthu omwe anasemphana
ndi zipolopolo”—Anthu omenyera ufulu wawo omwe anapulumuka pankhondo yolimbana ndi
atsamunda komanso amene anapulumuka ku maulamuliro ena omwe anayamba kulamulira
pambuyo pake.
“Ukuwadziwa eti?”
“Ayi, ndinangomva mbiri yawo.”
“Kodi anthu omenyera ufulu ndi ndani?” Muriuki anafunsa.
34