Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 33
Matigari
Madalaivala anaima aja nawonso anapitiriza ulendo wawo.
Eni maokala anapitiriza kugulitsa malonda awo ndipo ogwira
ntchito kufakitale anapitirizabe kuyenda kwinaku
akukambirana nkhani zomwe zinkachitika pafakitaleyo. Iwo
ankakambirana za kunyanyala ntchito komwe ankafuna
kuyambe kuchitika masana a tsikulo. Analibe nazo ntchito zoti
mdala anagendedwa koopsa uja anali kwala pansewu, ali
chikomokere.
Mwana anathawa uja, anatulukira atagwira dzanja munthu
wina yemwe ankagwira ntchito pafakitaleyo ndipo ankasonyeza
munthuyo bambo anali chigonere pansi uja.
“N’chifukwa chiyani akutuluka magazi chonchi?” munthuyo
anamufunsa mwanayo pamene ankatulutsa kansalu kopukutira
mamina n’kuyamba kusunsa magazi pachipumi komanso
pakhutu la bamboyo.
Bamboyo anatsitsimuka ndipo atangotsegula maso, anaona
mwana uja akuoneka wachisoni zedi.
“Mwana wanga, zikomo kwambiri kuti sunandisiye
ndekha?” bamboyo anatero.
“Ayi,” mwanayo anakana akuyang’ana pamene magazi a
bamboyo anayenderera.
“Sindidzakuiwala mwana wanga,” bamboyo anatero.
Kenako anazindikira kuti mwanayo anali limodzi ndi munthu
wina yemwe ankamupukuta magazi pankhope yake.
32