Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 32
Matigari
Bamboyo ankadzifunsa mafunso ambirimbiri koma
sankapeza mayankho. Mafunso onsewo ankangoloza ku funso
lalikulu limodzi lakuti, “Kodi ndi ndani watipepetula kuti
tiyambe kumenyana tokhatokha? Ndi ndani amene wapereka
temberero kuti ana ndi makolo awo azimenyana, mdani wawo
akuwonerera mosangalala.”
Chimene chinkamuteteza kuti mwala usamufike chija
chinakhala ngati chamusiya tsono. Kenako mwala
unamugagada pakhutu lakumanja. Ankangomva ngati khutulo
lathothokapo. Ataligwira, dzanja lake lonse linanyowa ndi
magazi. Mwala wina unafikira m’mutu ndipo unanyamula
chipewa anavala chija n’kukachigwetsera kumbuyo kwake.
Kenako anatembenuka n’kuwerama kuti achitole. Pamene
ankaweramuka, mwala wina unamukang’antha pachipumi.
Anamva ululu woopsa moti anataya pansi chipewa komanso
chijasi chija.
Iye ankatha kumva zitseko za magazi zikutseguka komanso
ululu woopsa ukukolera ngati moto kumutu kwake. Mtsinje
wamagazi unafwamphukadi kuchokera m’mphuno, m’kamwa
komanso m’makutu mwake. Ana aja ankangokhala ngati agalu
olusa omwe akukanganirana nyama moti anayamba kuvunga
matalala a miyala kwa bambo uja. Ankangokhala ngati akupha
galu wachiwewe. Miyala yonseyo inatera pa bambo uja moti
nkhope yake inakupukakupuka. Kenako anagwera pansi ngati
thumba la mbatata, n’kukomoka. Mtsinje wa gulu la ogwira
ntchito kufakitale aja unafika pamene bamboyo anagwera ndipo
gululo linakhala ngati lamumiza. Gulu la ogwira ntchitowo
linkangoyenda ngati palibe chimene chimachitika. Ana aja
anasiya kamodzim’kamodzi kugenda ndipo anabwerera
kumudzi wawo.
31