Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 29

Matigari onse. Bamboyo anadzifunsa kuti, “Zomwe zinkachitika kale zija si izi zikuchitikanso lerozi? Zinkachitika kale, zikuchitikanso masiku ano. Kodi tidzasiya liti kuona malodza amenewa?” Mtima wake unapopa magazi mwamphamvu ndipo zinkangokhala ngati nawonso ubongo wake ukuchita zomwezo. Iye ankangolakalaka atakumbatira ana onse n’kuwatenga kupita nawo kunyumba yake nthawi yomweyo. Iye ankafuna kutenga anawa n’kupita nawo kunyumba ija yomwe iye ndi Mtsamunda Williams anakhala akumenyanirana zaka zapitazo. Nyumba yomwe inachititsa kuti azikhala moyo wothawathawa m’mapiri komanso m’nkhalango. Anadzifunsa kuti, “Kodi panja tinkaimba nyimbo iti? Timagawana ngakhale nyemba imodzi, yomwe yagwa pansi panthaka. Nyemba imodzi yomwe tinaivutikira . . . ” Iye ankadziona akulowa nyumba yake ija limodzi ndi ana ake, akuyatsa moto komanso akugwira ntchito zapakhomo limodzi, utsi ukutuluka m’chumuni cha nyumba yawo. Iye anatsimikiza mtima kuti anawo adzachoka kumanda a galimoto ankakhalawo komwe ankakhala moyo wozunzika kwambiri. Iye ankaona kuti anawo ayenera kuyambanso kukhala moyo wabwino, osati womangodyeredwa masuku pamutu. Ankafuna kuti anawo akakhale m’nyumba yatsopano. Malo abwino ngati paradaiso. Koma kenako m’mutu mwake munabwera maganizo ena. “Zimenezitu zitheka! Palibe chimene chingalake anthu amanja omwe akuchita zinthu mogwirizana.” Pamene ankaganiza zimenezi, anangopezeka kuti akuyenda kulowera kunali ziphapha zagalimoto zija kuti akawauze anawo zimene ankaganizazi. Kuti zinthu zidzasintha ndipo padzikoli 28