Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 272
Matigari
*Sisi mbwa kali. (Kiswahili): Kutanthauza " Ndife agalu olusa."
Mwadzidzidzi, kunaoneka zing'aning'ani, ndipo ziphaliwali
zingapo zinawomba. Kenako madontho angapo amphulupulu
anayamba kuthonya. Posakhalitsa chimvula chinayamba
kupwatamuka koopsa.
Gulu la asilikali komanso apolisi lija linafika m'mbali mwa
mtsinje muja. Ena anali adakali pamsana pamahatchi ndipo ena
anangoimaima.
Ankaoneka kuti anali ndi njala yaikulu yogwira munthu.
Koma chifukwa cha zimene zinachitikazi mkwiyo unawayakira
chifukwa anati atataya ndalama yokwana mapaundi 5,000,
omwe anali atangogwera kumene mumtsinjewo. Apa n’kuti
mtsinjewo ukukukuma ndi madzi omwe anadzadza chifukwa
cha chimvula chija.
Iwo anayenda m'mbali mwa mtsinjewo akuganiza kuti aona
matupi a Matigari ndi Guthera akuyandama pamwamba pa
madzi kapena atatsakamira penapake. Ankadzifunsa kuti, ‘Kodi
afadi kapena athawa? Kodi Matigari ndi ndani kwenikweni?’
Mvulayo inakhuthuka koopsa ngati kuti zitseko
zakumwamba zatseguka ndipo madontho ake ankangokhala
ngati akuchokera mundowa.
Kungochokera nthawi imeneyo, mphekesera zinkamveka
kuti mvula imene inagwayo ndi imene inazimitsa moto wonse
womwe unayatsidwa ndi magulu a anthu olusa aja. M'madera
onse a m'dzikoli, ana anatuluka panja n'kuyamba kuimba kuti:
Mvula, mvula bwera lero,
kuti ndikuphere mwana wang'ombe.
Ndi winanso
wokhala ndi mabelu m’khosimu!
271