Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 271
Matigari
Matigari ankatha kumva phokoso la madzi a mumtsinje uja
bwinobwino tsopano. Masitepe angapo ankanalumphira
mumtsinjemo . . . ndipo akanawolokera tsidya lina . . . Koma
atangotsala pang'ono penipeni kuti alumphe, agalu ena
anamuwakha.
Ena onse anabwera n'kuwaunjirira. Agaluwo anakhadzula
Matigari ndi Guthera mwankhanza kwambiri. Anang'amba
zovala zawo komanso minofu yawo ndi mano awo okhala ngati
misomali. Koma ngakhale nthawi imodzi, Matigari sanasiye
Guthera ngakhale pang'ono. Magazi awo anali chuchuchu ndipo
ena analowa munthaka pafupi ndi mtsinje uja.
Apolisi komanso asilikali anali pamahatchi aja
anathamangira kunali agalu kuja. Ngakhalenso aja ankayenda
wapansi analiyatsa liwiro, kunjonjola kuti akakhale oyamba
kugwira munthu ankafunidwa kwambiriyo. Matigari
anasonkhanitsa mphamvu zake zonse ndipo atagwirabe Guthera
m'manja mwake, anayamba kukwawa ndi mawondo ake
kulowera kunali mtsinje kuja. Pamene ankakwawapo n'kuti
agalu ena omwe anali atagagada mwamphamvu miyendo
komanso matako ake akukhwekhwerekera pansi. Agaluwo
ankakhala ngati apana nyama yoti adye, moti ankalolera
kukhwekhwerezedwa pansi koma sanamusiye.
Kenako Matigari ndi Guthera anagwera mumtsinje.
Madzi anathovokera m'mwamba ndipo ena anagwera
m'mbali mwa mtsinjewo momwe munali mouma gwa.
Kenako agalu aja anaima m'mbali mwamtsinje muja,
malilime ali lawilawi ngati alandidwa nyama. Ena ankasetekera
magazi omwe anali pamphuno zawo. Ndipo ena ankalira
mwaukali kwambiri ngati akuuza dziko lonse kuti: Sisi m bwa
kali.*
270