Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 270
Matigari
Atangochita zimenezi panamveka phokoso loopsa la mifuti.
‘Mayo!’ Guthera anakuwa n'kugwera pansi. Matigari ndi
Muriuki anadziponyeranso pansi, koma sanavulale.
"Pitirizabe kukwawa! Koma uzikwawa molowera uku ndi
uku!" Matigari anamuuza Muriuki. "Muriuki, fulumira
ukawoloke mtsinjewo, ndipo ukandibweretsere mfuti yanga ya
AK47 yomwe ndinaikwirira pansi pa mtengo wakachere.
Fulumira, uchite chilichonse chomwe ungathe kuti
undibweretsere mfutiyo!"
Muriuki anapitiriza ulendo. Iye ankathawa molowera uku
ndi uku. Nthawi zina ankagwa, kugubuduka, koma
ankadzukanso n'kuyamba kuthawa kumalowera kunali mtsinje
kuja. Kenako anawoloka.
Guthera anali akulirabe. Iye anawomberedwa pamwendo
wakumanja ndipo mwendowo unkachucha mtsinje wamagazi.
"Zipitani! Zipitani musavutike nane!" Guthera anauza
Matigari. "Ndisiyeni ndifere pompano!"
Koma Matigari anamunyamula m'manja n'kuyamba
kuthawa naye molowera kunali mtsinje kuja. Agalu komanso
asilikali aja anali atayandikira kwambiri. Mfuti zinkamveka
ponseponse, kuchokera mbali zosiyanasiyana.
Zinkaoneka kuti Matigari ankatetezedwa ndi mphamvu
inayake yapadera chifukwa palibe chipolopolo ngakhale
chimodzi chomwe chinatera pathupi lake . . . Zinkangokhala
ngati kuti pamene zipolopolozo zinkafika pa iye, zinkasanduka
madontho a madzi.
Kutsogolo kwake kunali mtsinje. Mtsinjewo unali pafupi
kwambiri . . . mwina mapazi owerengeka chabe . . . Agalu aja
anali akukuwa kumbuyo kwake.
269