Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 27

Matigari “Ayi, ndinawasiya ndi ineyo. Choyamba ndinalandidwa nyumba yanga, kenako ana anga anabalalikira mbali zosiyanasiyana za dziko lino.” “Zinachitika liti zimenezo?” “Ii! Kalekale, kale kwambiri.” “Ndiye munali kuti zaka zonsezi? N’chifukwa chiyani simunaganize zowafunafuna zaka zapitazo?” Bamboyo anamezera mate. Ankasinkhasinkha kuti amuuza bwanji mwanayo kuti wakhala akulimbana ndi atsamunda kuti amubwezere nyumba yake! Ankaganizira kuti amufotokozera bwanji kuti kwa zaka zosawerengeka wakhala akulimbanana ndi Mtsamunda Williams n’cholinga choti ana ake asazunzike. Kenako anaganiza zouza m’nyamatayo mavuto omwe anakumana nawo pamoyo wake pamene ankalimbana ndi Mtsamunda Williams n’kumakhala moyo wothawathawa m’nkhalango, kumabisala m’mapiri, m’zigwa, m’mapanga, mitsinje komanso malo ena osiyanasiyana. “Ndinayamba kuwasakasaka zaka zapitazo.” Bamboyo anaitumbula motero nkhaniyo, koma pamene ankati adziiphinya, Muriuki anasintha nkhani. “Koma mungawazindikire mutakumana nawo?” “Amaoneka ngati iweyo, komanso anthu ena onse. Moti iweyo ukungooneka ngati unabadwa bere limodzi ndi ana anga. Zikungokhala ngati munabadwa kwa mayi m’modzi, bambo m’modzi.” “Inetu bambo anga anamwalira,” anatero mwanayo. “Ndinamva zoti anaphedwa pamene ankamenyera ufulu wa dziko lino.” 26