Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 269
Matigari
aja kunawayandikira kwambiri. Kuchokera pamene analipa
kukafika panali mtsinjewo, panali malo ena opanda mitengo.
"Ngati titakwanitsa kuwoloka mtsinje mukuuona apowo,"
anatero Matigari, "adani athuwa satigwiranso. M'nkhalango
mukuziona ukozo tikayatsa moto waufulu wathu. Ufulu wathu
wodzilamulira womwe tinamenyera nkhondo polimbana ndi
atsamunda unagulitsidwa ndi atambwali ena omwe
atsamundawo anawaika pampando!"
Kenako anazindikira kuti amasakidwasakidwa kuchokera
mbali zonse. Gulu la agalu omwe ankawalondola kuchokera
kumbuyo kwawo ankangokhala ngati gulu la nkhosa. Matigari
anakumbukira mmene Mtsamunda Williams ndi anzake
ankachitira akamakasaka nkhandwe zaka zambiri zapitazo.
"Chimene chatsala kuti afanane ndi Mtsamunda Williams
ndi mahatchi basi," Anatero Matigari akuganizira kuti achite
zotani kuti akawoloke mtsinje uja.
"Ogo! Taonani!" Muriuki anakuwa. "Alitu ndi mahatchi!"
Zinali zoonadi, kumanzere komanso kumanja kwawo kunali
apolisi apamahatchi, ndipo apolisiwo ankatsatira gulu la agalu
aja. Ndipo kumbuyo kwawo kunali apolisi enanso ambirimbiri
omwe ankayenda wapansi, nawonso atagwira zingwe za agalu
awo.
"Ifeyo ndiye nkhandwe zawo," Matigari anawauza choncho.
"Tiyenera kuyamba kuthamanga ngati nkhandwe tsopano.
Tikamathawa tizilowera uku ndi uku kuti tiwasokoneze.
Mwakonzeka? Chabwino, tiyeni!"
Kenako anadzambatuka pamene anabisala panja n'kuyamba
kuthamangira kunali mtsinje kuja. Kulephera kukafika
kumtsinje umenewu kukanatanthauza kutaya moyo wawo.
268