Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 264

Matigari Tiyeni tiwotche ndende zomwe mwatsekeredwa ophunzira-tiwotchee! Tiyeni tiwotche ndende zomwe mwatsekeredwa ophunzira-tiwotchee! Tiyeni tiwotchee Parrotology-tiwotchee! Tiyeni tiwotchee Parrotology-tiwotchee! Tiwotchee, tiwotchee! Tiwotche! Tiwotchee, tiwotchee! Tiwotche! Koma ngakhale zimenezi zinkachitika, aliyense ankadzifun- sa kuti: ‘Kodi Matigari ma Njiruungiyo ali kuti?’ Wotsogolera apolisi uja analamula anzake aja kuti aletse kha- lidwe lootcha zinthu linayambikalo. Posakhalitsa apolisiwo anayamba kuwombera m’mwamba. John Boy Junior atamva zoti nyumba yake ikuwothedwa, anagwa pansi n’kukomoka. Anthu ena anamutenga n’kutha- mangira naye kuchipatala. Iye anakomoka chifukwa ankadera nkhawa kwambiri kuti mkazi ndi ana ake adzafikira pati aka- bwera ku USA komwe anapita kutchuthi. Sikuti ndi John Boy yekha amene ankazunzika ndi maganizo angati amenewa. Anthu ena ogwira ntchito ndi makampani akunja nawonso sadatione tulo patsikuli. Iwo ankaona kuti zimene zinachitika usikuwo zinachita kulinganizidwa bwino. Komabe ankadzifunsa kuti: ‘Kodi Matigari ndi ndani kwenikweni? Kodi kumeneku kunali kuyambika kwa nkhondo ina yolimbana ndi ulamuliro? Nkhondo yofanana ndi imene inamenyedwa kalekale m’thawi ya atsamunda? Nanga n’chifu- kwa chiyani apolisi sanawombere anthu omwe ananyamula mo- to n’kumayatsa zinthu? Kodi zinatheka bwanji kuti Matigari awasokoneze mpaka kukafika kunyumbako?’ Pamapeto pake 263