Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 263

Matigari Katundu yense wa anthu obera osauka ayakee! Katundu yense wa anthu obera osauka ayakee! Parrology nayenso ayakee! Parrology nayenso ayakee! Chikhalidwe cha parrotology tikuti chiyakee! Chikhalidwe cha parrotology tikuti chiyakee! Tsankho komanso kuponderezana kuyakee! Tsankho komanso kuponderezana kuyakee! Anthu aja anapengeratu moti anayamba kuyatsa ma Mer- cedes-Benz omwe anali pamalowo. Eni magalimotowo anatha- wa pofuna kupulumutsa miyoyo yawo. Magalimoto a mtundu- wu omwe anapulumuka anali omwe anaimikidwa pafupi ndi nyumba ija komanso kufupi ndi nsewu. Anthu aja anagawika m’magulumagulu ndipo anabalalikira mbali zosiyanasiyana n’kuyamba kukoleza nyumba komanso minda ya tiyi ndi khofi. Apolisi anagwira njakata ndipo ana- lephera kuletsa khamulo. Anthuwo anayatsa nyumba. Anayatsa minda yatiyi. Anayatsa minda yakhofi. Komanso anayatsa magalimoto. Pamene ankachita zimenezi, ankaimbanso mokweza kwam- biri moti zinkangokhala ngati akumenya nkhondo yolimbana ndi anthu omwe ankawachitira nkhanza: Tiyeni tiwotche kumangidwa popanda mlandu-tiwotchee! Tiyeni tiwotche kumangidwa popanda mlandu-tiwotchee! Tiyeni tiwotche kuthamangitsa omenyera ufulu wathu-tiwotchee! Tiyeni tiwotche kuthamangitsa omenyera ufulu wathu-tiwotchee! 262