Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 262

Matigari khamulo likhoza kuwaukira komanso kuyamba kubutsa moto nyumba za anthu ena m’deralo. Kenako kunamveka phokoso loswa makutu kuchokera kunali nyumba ija. Tizidutswa komanso maduka anaulukira m’mwamba ndipo zina zinagwera m’mitu mwa anthu ankaimba aja. Zinkangokhala ngati nyumbayo yaphulitsidwa ndi bomba. Inali Mercedes-Benz ija yomwe inaphulika ndipo inangow- onjezera malilime a moto omwe ankauluka kuchokera m’nyum- ba inkapsa ija. Malilimewo anagwirana n’kupanga chimoto chachikulu cho- lusa. Motowo unkayaka kumpanda wonsewo, m’minda ko- manso malo ena ozungulira. Ndi ana aja omwe anayambitsa zochitika zina zomwe zi- natsatira. Anayamba kukuwa kuti, “Ngakhalenso nyumba zinazi ziyakee, ziyakee, ziyakee!” Kenako nyimboyo inasintha kolowera: Chilichonse chomwe ndi cha akapolo chiyakee! Chilichonse chomwe ndi cha akapolo chiyakee! Khofi wawo ayakee! Khofi wawo ayakee! Tiyi wawo ayakee! Tiyi wawo ayakee! Khwimbi la anthu lija linapala moto uja ndipo nalonso lina- yamba kuimba mwachimvano cha mavu kuti: Galimoto zawo ziyakee! Galimoto zawo ziyakee! Galimoto zonse za anthu ankhanza ziyakee! Galimoto zonse za anthu ankhanza ziyakee! Ngakhalenso za antchito awo, ziyakee! Ngakhalenso za antchito awo, ziyakee! 261