Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 261
Matigari
zimenezi moti analepheratu kuletsa khamulo, lomwe linkayen-
da ngati madzi osefukira.
“Nyumba ya Boy ikuyaka! Nyumba ya Boy ikuyaka!” ankaimba
choncho.
Anthu ena ankafuna kulowa m’nyumbayo kudzera pawin-
do lomwe silinkatuluka utsi. Iwo ankafuna alowe m’nyum-
bamo n’kukaba katundu. Aliyense ankafuna kuti atengemo ke-
nakake, ngakhale kochepa bwanji.
“Nyumba ya munthu woipa Boy ikuyaka! Nyumba ya munthu
woipa Boy ikuyaka!” chuni cha nyimbo ija chinayamba kusintha.
Utsi woopsa womwe unayamba kutuluka m’nyumba ija
unabweza anthu omwe ankafuna kulowera pawindo aja.
Malilime a moto walawilawi ankathamuka kuchokera mkati
mwa nyumbayo n’kumagwera panja. Khamu la anthu aja lina-
yamba kubwerera m’mbuyo, ndipo anaima mozungulira
nyumbayo mofanana ndi mmene anthu amachitira ak-
amapereka mpata kwa anthu omwe akukutumulana. Iwo
anapitirizabe kuimba:
Motoo, moto wayakaa, moto wayakaa, moto wayakaa.
Tiyeni tiwothe motoo, moto wayakaa, moto wayakaa.
Motoo, moto wayakaa, moto wayakaa, moto wayakaa.
Tiyeni tiwothe motoo, moto wayakaa, moto wayakaa.
Iwo anaima mozungulira nyumbayo akuimba mwam-
phamvu nyimboyi ndipo ena ankakuwa kuti, “Nyumba ya Boy
ikuyakaa . . . ”
Wapolisi ankatsogolera anzake uja anaitanitsa wapolisi
wina yemwe ankayankhula ndi wailesi meseji uja. Mkulu wa
apolisiyo anaitanitsanso apolisi ena chifukwa zinkaoneka kuti
khamu la anthulo likhoza kuwapweteka. Iwo ankaopa kuti
260