Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 260

Matigari Wapolisi uja anabwerezanso chilengezo anapereka chija. "Matigari, tikudziwa kuti uli m'nyumbayi. Ingodzipereka. Ingogonja basi! Palibe amene atakuvulaze. Uwauzenso anzako uli nawowo kuti achite chimodzimodzi. Koma ukapanda kungogonja, uphedwa. Takuzungulirani mbali zonse. Palibe ku- mene mungathawire. Enanu ngati mukundimva ingodziperekani, musamumvere Matigari." Pamalowa pankawala zedi chifukwa cha magatsi anali panja pa nyumba ija komanso matochi a apolisi aja. Kenako asilikali aja analowa kumpanda kuja n'kumayenda chozemba kulowera kunali nyumba kuja. Ena ankati kuthamanga, n'kukaima kaye kuseri kwa mtengo, galimoto kapena maluwa. Ankachita zime- nezi kuti zigawenga zinali m'nyumba ija zisawaone. Ankaganiza kuti zigawengazo zinali ndi zida zoopsa. "Kaya usankha kuchita chiyani, dziwa kuti suthawa. Limene- li ndi chenjezo. Ndikukupatsa mphindi zisanu kuti ukhale uta- dzipereka; apo bii ndilamula asilikali kuti akuphe." Mphindi imodzi ikangodutsa, wapolisi uja ankaperekanso chenjezo: "Wangotsala ndi mphindi zinayi." "Watsala ndi mphindi zitatu." "Mphindi ziwiri." "Mphindi imodzi." Kenako mwadzidzidzi moto wamphamvu unaphulika ku- chokera pawindo lanyumba ija. Kuphulikako kunangokhala ngati kunatsegula pakamwa pa anthu aja. Iwo anayamba kuku- wa komanso kuchita mavuvu. Anthuwo anayamba kukhamu- kira kunali nyumba ija. Asilikali aja anadzidzimutsidwa ndi 259