Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 256
Matigari
Magalimoto a apolisi aja anapitirizabe kumulondola. Matig-
ari ankatha kuwaona pagalasi loonera zinthu zakumbuyo. Ko-
ma anazindikira kuti ngakhale kuti galimoto za apolisiwo zi-
nali zaliwiro kwambiri, apolisiwo sankayerekeza ku-
muyandikira kwambiri. Iye anamvetsa chifukwa chake. Iwo
ankaganiza kuti ali ndi mfuti. Iye anadziuza kuti, ‘Si paja
pawailesi analengeza kuti anthu omwe aba galimotoyo ali ndi
zida zoopsa?’ Matigari anafuna kuseka. Koma pamene
kusekako kunkati kuziyambika, mkwiyo unamubwerera ata-
dziwa kuti apolisi atseka njira zonse zomwe akanadutsa kuti
akafike kumene anakwirira zida zake kuja.
Matigari anatsimikiza mumtima mwake kuti zivute zitani,
salola kuti Boy amubere tsogolo lake lonse. Koma ankadzifunsa
kuti, ‘Kodi ndikafika bwanji kumtengo wakachere uja?’
Koma kenako anatsimikiza mumtima mwake zinthu zimene
ankafuna kuchita. Nyumbayo inali yake. Ankadziuza kuti an-
zeru ndi amene amapambana. Anaona kuti angotengera
chitsanzo cha zimene a Iregi anachita poukira boma.
Kenako anatenga msewu wolowera kumene kunali nyumba
kuja. Apolisi aja anapitirizabe kumulondola, atayatsa magetsi
apadenga la galimoto zawo ndipo nyalizo zinkangokhala ngati
zikuzungulira mumdima womwe unali madzulowo. Masailini
anali pokopoko kumveka mwaphokoso kwambiri.
Iye anadabwa kwambiri pamene anatulukira munsewu
womwe unkalowera komwe kunali nyumbayo. Zinkangokhala
ngati anthu a m'dziko lonselo asonkhana kunyumbako. Gal-
imoto zinali zitaimikidwa mbali zonse. Panalibiretu malo omwe
munthu akanaimika galimoto yake m'mbali mwa nsewuwo.
Kumalowa kunali fumbi. Nawonso asilikali anali yakaliyakali
paliponse atanyamula mifuti ndi matochi. Magetsi a panja
255