Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 255
Matigari
pakati kuti asowe kothawira. Apolisiwo ankaganiza kuti aka-
muopseza achita mantha n'kulowetsa mateyala ake m'ngalande
zomwe zinali m'mbali mwa nsewuwo kapena kungoima. Ke-
nako mosamala kwambiri, Matigari anaponda buleki, ndipo
ankawonjezera moto pang’ono kuti galimtoyo isangoima ka-
modzinkamodzi. Galimoto za apolisi zija nazonso zinabweza
moto chifukwa ankaganiza kuti Matigari akuima. Komatu apa
Matigari ankangodzikonzekeretsa! Iye anayamba watsimikizira
kaye kuti panalibenso galimoto ina kuwonjezera pa awiriwa,
imene inkabwera.
Ataona kuti ndi ziwiri zomwezo, anatembenuka mwadzidzi-
dzi ndipo anayamba kuyendetsa galimoto molowera kumene
ankachokera kuja.
Apolisiwo anadzidzimutsidwa kwambiri, ndipo posakhalitsa
anangozindikira adyana okhaokha. Pamene ankafufuza kuti
chikuchitika n'chiyani, Matigari anali atatha mtunda.
Kenako magalimoto awiri aja anayamba kumuthamangitsa.
Iye ankadzifunsa kuti, ‘Kodi akapolo amenewa adziwa bwanji
kuti ndine ndikuyendetsa galimoti imeneyi? Kodi mwina
kazitape uja ndi amene wawauza?’ Kenako anakumbukira kuti
mkazi wa nduna uja anakanena kupolisi kuti galimoto yake
yabedwa. Mzimayiyu anachita mwayi chifukwa munthu
ankachita naye zopusayo anali dalaivala wake osati munthu
wina wapadera. Akanakhala munthu wina, akanaganiza kawiri
asanakanene kupolisi kuti galimoto yake yabedwa. Komabe
mwina akananena kuti munthu amene anali nayeyo
anangokwera nawo galimotoyo basi. Matigari anadziuza kuti,
‘Kodi nanenaso ndikuganiza chiyani? Kuganizira zimenezi
sikungandithandize mpang’ono pomwe. Ukaziputa limba.
Mwana wang’ona sakulira dziwe limodzi!
254