Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Página 254

Matigari wamwamuna. Galimoto ya apolisi inkangomulondola. Zinali zoonekeratu kuti inkathamangitsa iyeyo. Ataona izi, Matigari anaponda latalata ndipo kunali kuthamangitsana. Matigari sankadziwa choti achite. Iye ankafuna ataimitsa galimotoyo kenako n'kuyamba kuthawa wapansi kupita kunk- halango kuja. Koma ankaona kuti akhoza kugwidwa. Iye anayamba kukayikira komanso kudziimba mlandu. Ankaona kuti akanachita bwino akanayamba wapita kunyumba kuja. Ko- ma ankadziuza kuti, ‘Ndiye ndikanatenga bwanji chinthu chom- we ndinachikhetsera thukuta m'manja mwanga mulibe chida?’ Galimoto ya apolisi ija inayamba kuyandikira. Matigari anapitirizabe kuponda moto, iye ankafuna kuchita zinthu zoti awasokoneze apolisiwo. Zikanakhala kuti panali msewu wina wam'mbali, akanatenga umenewo. Koma ankadzifunsa kuti, ‘Nanga bwanji nsewuwo utakhala kuti watha kutsogoloko?’ Ko- mabe sanataye mtima. Iye anapitirizabe kuyang’ana m'mbali mwa nsewuwo kuti mwina aona penapake poti angakhote. Ankaganiza kuti mwina apeza penapake poti akhoza kutembenuka, mwina pamene msewu ukukhota kapena palan- dabauti. Mwadzidzidzi, anangozindikira kuti galimoto ina yatulukira kutsogolo kwake. Galimoto imeneyinso inali ya apolisi. Apatu anali pampanipani, pakati pamagalimoto a apolisi awiri omwe ankamuthamangitsa. Koma kodi akanathawa bwanji? Magetsi a pamwamba pa galimoto ya apolisi anayamba ku- wala. Nawonso apolisi aja anayamba kumuunika ndi matochi awo, n'kumamupatsa chizindikiro choti aime. Galimoto inali kutsogolo kwake ija inkayenda mbali yofanana ndi imene Matigari ankayenda ija, ndipo kumbuyo kwake kunali ina yomwe inkamutsatira ija. Iwo ankafuna kuti akumane naye 253