Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 253
Matigari
Munthu aliyense ali ndi manja ake, ayenera kumawag-
wiritsa ntchito m'malo mongowalongedza m'thumba n’ku-
mayembekezera kuti ena amugwirire ntchito.”
Mawuwa anakhala ngati apanga nyimbo m'maganizo
mwake. Iye ankaimba nyimboyi mobwerezabwereza.
Pamene ankaimba nyimboyi, anakumbukira zimene
anakambirana ndi Ngaruro wa Kiriro. Ngaruro anamuuza
kuti m'dzikomo munali magulu awiri a anthu. Panali gulu la
anthu olamulira mopondereza anzawo komanso mamesen-
jala awo, oyang'anira, apolisi ndi asilikali. Chipani cholamu-
la ndi chimene chinali mamesenjala amenewa ndipo ndi
amene ankalamulira boma, malamulo komanso asilikali.
Mfundo komanso chikhalidwe ndiponso mbiri yadziko,
yomwe inkalembedwa inali m'manja mawo chifukwa iwowo
ndi amene ankanyamula uthenga . . . Kumbali inayi, kunali
gulu la anthu ogwira ntchito, ali ndi zimene amakhulupirira,
chikhalidwe chawo komanso mbiri yawo. Mamesenjala
achipani cholamula aja ankayesetsa kutseka pakamwa mbiri
ya ogwira ntchitowa pomanga anthu ake n’kumaka-
watsekera kundende kuti zoona zenizeni zisadziwike. ‘Kodi
zimenezi zichitika mpaka liti,’ anadandaula Ngaruro, ‘Kodi
anthu apirira ulamuiro wa mamesenjala komanso mabwana
awowa mpaka liti?
‘Mpofunika chilungamo chioneke! Chioneke kwa anthu
amene akuponderezedwa,’ Matigari anadziuza choncho. In-
de chilungamo chimapita kwa oponderezedwa ngati atachita
zinthu mogwirizana kwinaku atatenga zida n'kumalimbana
ndi adani awowo . . . Kenako anayang'ana pagalasi loonetsa
zinthu zam'mbuyo. Anazindikira kuti m'mbuyo mwake
mukubwera mbola. Kenako anaponda moto mwana
252