Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 252
Matigari
Gawo 19
Matigari analowa mumsewu waukulu. Pa nthawiyi n'kuti
kunja kutayamba kuvala m’dima. Iye anaponda latalata, ndipo
mwendo wake unaponda m’mafuta moti galimotoyo inaulukira
m’tsogolo. Matigari ankaganizaganiza kuti apite kunyumba kuja
komwe anthu anasonkhana kuti akawaone zimene zikuchitika.
Koma kamtima kena kankamuletsa kuti akatenge kaye zida
zake. Iye sanalole kuti chiyeso choti akaone athuwo chimu-
gonjetse. Ankaona kuti chilungamo chimabwera kwa oponde-
rezedwa ngati anthuwo atachita zinthu mogwirizana n'kuyamba
kulimbana ndi adani awowo ndi zida. Iye anali atamasula kale
lamba wamtendere. Ankafuna abwerere kunkhalango kuja
n'kukavala lamba wake wazipolopolo kuti akalimbane ndi adani
ake. Ankaona kuti akapanda kuchita zimenezi ndiye kuti anthu
ake asowa kolowera, asoweratu mtengo wogwira. Ankadziwa
kuti si nzeru kuti apitirizebe kukhetsa thukuta lake n'kumapin-
dulitsa nthata zosayamika zomwe zimangokolola pamene
sizinalime. Iye ankayembekezera kudzaona tsiku limene mavuto
onse adzathe. Kungoti sankadziwa kuti zidzachitika liti.
Ankayembekezera kuti nthawi idzafika pamene:
Omanga azidzakhala m'nyumba zapamwamba,
Atelala azidzapha ulusi,
Alimi azidzadya zakudya zonona.
‘Ayi, si chilungamo kuti anthu apitirize kukhetsa thukuta
kuti apindulitse nthata zomwe zimakolola pomwe sizinafese.’
Mumtima mwake anatero.
Ife matelala sitikufuna kuti tisanduke mapoto omwe amaphi-
ka koma osadya nawo.
251