Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 251

Matigari Maso awo anaphana. Anali Giceru, kazitape uja, munthu yemwe uja anamangidwa naye limodzi m'ndende. Matigari anamuona akuyankhula ndi munthu wina wog- wira ntchito pagalaja. Ndipo anthu awiri onsewo anayamba kuyenda molowera kumene kunali galimoto kuja. Matigari anayamba kudya mapulani. Panalibenso galimoto ina pamalowa. Choncho njira yokhayo imene anthuwa akanalu- mikizana ndi anthu inali kudzera palamya basi. Kenako ana- manga mfundo imodzi. Anakwera m'galimoto ija, kuliza injini n'kuyamba kuyendetsa. Iye ankadziuza kuti, ‘Kazitapeyu akhoza kuchita chilichonse chimene akufuna. Munthu amafa kamodzi basi!’ Posakhalitsa Giceru anaimbadi foni. 250