Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 250
Matigari
“Anthu akukhulupirira kuti munthu wina wotchedwa
Matigari ma Njiruungi yemwe wathawa kuchipatala cha anthu
amisala m'mawa wa lero, akufuna kupita kunyumba kwa Boy
kuti akailande mwachiwawa. Apolisi akufuna akamugwire an-
thu onse akuona. Ngati mutandifunsa ineyo kuti ndikuuzeni
maganizo anga, ndikhoza kukuuzani kuti munthuyo si
wopenga.”
“N’chifukwa chiyani mukutero? Munthu wake ndi wotani?”
“Anthu ena akumanena izi, ena akumanena izi. Ena
akumanena kuti ndi wamtali komanso wooneka ngati chiphona
ndipo ena akumati ndi wamtali moti akhoza kugwira kumwam-
ba. Ena akumanena kuti ndi wamfupi ngati chitsa, pomwe ena
akumanena kuti ndi mwana. Palibe amene akudziwa kuti mun-
thu ameneyu ndi wamtundu wanji. Zikumvekanso kuti amatha
kuyankhula zinenero zosiyanasiyiana. Ndinamva ena akunena
kuti munthu wake amakonda kuyenda yekha. Pomwe ena
akumanena kuti nthawi zonse akumayenda ndi mwana ko-
manso akumatsatiridwa ndi mzimayi. Akumati ukhoza ku-
muona, koma kenako kungozindikira wasowa. Akumatsala ndi
mzimayi ndi mwana uja basi. Zikumamveka kuti ali uku, ena
akumati takumana naye uku. Akumapezeka paliponse. Ziku-
mavuta kuti ndiye munthu ugwire chiti. Zikanakhala kuti sin-
digwira ntchito ku kampani yogulitsa mafuta yakunjayi, bwenzi
nanenso ndili komweko.”
Matigari analipira ndalama ya mafuta aja ndipo anayamba
kuyenda molowera kumene kunali Mercedes-Benz kuja.
Asanatsegule chitseko chagalimotoyo, anaima kaye n'kuponya-
ponya maso. Iye anaona munthu anamuona akusuta fodya uja
akutuluka muofesi ija.
249