Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 247

Matigari Gawo 17 Zinali zoona kuti aliyense ankayembekezera kuona chozizwitsa tsiku limenelo. Asilikali komanso apolisi anali ponseponse. Iwo ankafuna kugwira Matigari wamoyo kapena wakufa. Ankafunitsitsa kuchita zimenezi anthu akuona. Anka- ona kuti zimenezi zipheratu mphekesera zonse zonena za zozizwitsa, angelo komanso kubweranso kwachiwiri kwa Khristu zomwe anthu ankazinena mosinjirira. “Ofunika tiwa- sonyeze anthuwa bwinobwino, awone ndi maso awo tiku- musenda chikopa Matigari amamutamayo,” mkulu wa apolisi analangiza apolisi anzake. Kunyumba kwa Robert Williams komwe John Boy anapita kukabisala kunali apolisi ambirimbiri olondera. Boy anakhala pafupi kwambiri ndi lamya n'cholinga choti akhale woyambirira kumva za kumangidwa kapena kuphedwa kwa Matigari. Ndipo mofanana ndi anthu ena onse, Williams komanso Boy, ankadikirira kuona chozizwitsa. Koma ankachita zimenezi kumtima kuli bi! John Boy ankatuluka thukuta m’kamwa. Atolankhani anyuzipepala zosiyanasiyana maso anali kun- jira, kudikirira kubwera kwa Matigari. Atolankhani a wailesi yakanema ankatutira zipangizo zawo kumalowa. Ndipo onse maso anali kunjira. Munthu aliyense yemwe anali kumalowa ankadikirira chin- thu chimodzi: Ankadikirira kuona chozizwitsa chikuchitika. Ko- ma pa nthawi yomweyo, onse ankadabwa. Ankadzifunsa kuti: Kodi Matigari ma Njiruungi ndi ndani kwenikweni? Kodi ndi munthu womenyera ufulu wadziko? Kodi ndi mngelo Gabrieli? Kodi ndi Yesu Khristu? Kodi ndi munthu wamnofu ndi magazi, kapena ndi mzimu? Kodi ndi mneneri woona kapena wabodza? 246