Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 245

Matigari Iye ankayankhula ngati akuwerenga zimene zalembedwa pachivundikiro cha mitima yawo. Kenako Matigari, Guthera komanso Muriuki anafutuka pang'ono n'kuchoka pamene ana aja anaima ndipo kenako anayamba kuyankhula monong'ona. Iwo ankakambirana zimene ankafuna kuti achite tsopano. Kenako Matigari anatulutsa ganizo lina. "Popeza kunyumbako kuli anthu ambiri tsopano, ndaganiza zoti tichite izi. Inuyo mupite kunyumbako, ndi ana ena onsewa. Ine ndipita ndikaone Mercedes-Benz ija pamene ndinaisiya. Ndikakaipeza pomwepo ndikaitenga n'kupita kukafukula zida zanga. Ndikakatenga zidazo ndikabwera kunyumbako kuti ndikathane ndi Boy. Panopa sindikuopanso kufa, kufera zinthu zathu!" "Nanga mukakapeza kuti Mercedes-Benz'yo kulibe?" Guthe- ra anafunsa. "Osadandaula. Ndibwerabe kunyumbako," iye anatero. "Ndinakuuzani chiyani? Boy sadzagonanso nyumba yomwe ndinamanga ine. Iyeyo ndi ineyo sitingagone nyumba imodzi usikuwu. Ndikuona kuti ndi bwino kumanga nyumba ina kuyambira pamaziko, nyumba yaikulu, nyumba yabwino ko- manso yolimba." "Ndiye fulumiranitu!" Guthera anatero. "Mukandibweretsere pistole!" Muriuki anawonjezera. Iye ankaganizirabe zimene anawonera mufilimu ya ma co w bo ys ku showo. Matigari ananyamuka, ndipo anawasiya onse akungo- muyang'ana. 244