Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 243

Matigari "Ayi!" "N'chifukwa chiyani simunatidzutse?" Matigari anafunsa, ndipo anayamba kukonzeka kuti anyamuke. "Zikanakhala bwino tikanabanduka kusanade," anatero kwa Guthera. Ana aja anaima mozungulira Matigari. Onse ankachita naye chidwi. Ena ankagwira zovala zake. Kenako anamubenthulira zimene zinkachitika. Anawo anamufotokozera kuti aliyense akupita kunyumba. "Nyumba yake iti?" "Nyumba ya Boy!" mwana wina anatero. "Eetu! Kunyumba!" wina anawonjezera. "Nanga akupita kumeneko kukatani?" Guthera anafunsa. "Kukumveka mphekesera zoti Matigari abwera lero. M'mawa womwewu mngelo Gabrieli, yemwe uja anamutulutsa m'ndende, amenenso anamutulutsa kuchipatala cha anthu amisala, ananena kuti abwera lero. Akutinso kukhala apolisi paliponse." "Mmene mumabwera muja n'kuti anthu ena atayamba kale kupita kunyumbayo," mnyamata wina anatero. "Iwo akufuna kukawona chozizwitsa!" winanso anatero. Ena anyamula maposita olembedwa kuti, "Tikaone Zoda- bwitsa." "Kodi ndiye kuti mukupita kumeneko?" "Inde, ndikupita." Matigari anayankha. "Ifenso tipita nawo," onse ananenera limodzi. "Tatiuzeni, kodi ndi inuyo amene aneneri ananena kuti adzabweraso kachiwiri?" mwana wina anafunsa. 242