Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 242
Matigari
. . . Sitima yonyamula zida zanyukiliya ya ku America yaima pa-
doko lina la ku . . . asilikali apanyanja okwana 10 sausande abwerera
kumtunda kuti akapumule pang'ono . . . Sitima zochokera ku South Af-
rica zanyamuka ndipo zikulowera ku Middle East. Meya wamzinda
wina womwe kunali sitimazi komanso makhansala ake anapita
kukatsanzikana ndi asilikali omwe anakwera sitimazi. Pamene ama-
tsanzikana nawo , meyayo anayamikira asilikaliwo kuti achititsa kuti
dera lawo litukuke pa nkhani zamalonda . . . Zikumveka kuti ama-
bizinezi ochuluka a m'tauniyo apha makwacha ambiri atagulitsa ma-
kondomu ochuluka zedi.
Malipoti ena ochokera m'tauniyo akunena kuti mtsikana wina wa-
baidwa ndi botolo lagalasi ndi chibwenzi chake, chomwe ndi msilikali
wa ku America. Mtsikanayo anafera pomwepo.
"Kodi n'chifukwa chiyani anthu a ku Americawa aman-
gopezeka paliponse padzikoli?" wina anatsirira ndemanga.
Guthera ndi Matigari anadzidzimutsidwa kutulo pamene
anamva kukuwa kwa Muriuki. Ana enanso anabwera kuti
adzaone chimene chachitika.
"Ndinalota ndili mundege," anatero Muriuki. "Koma kenako
inangosintha n'kukhala Mercedes-Benz. Kenako inasinthanso
n'kukhala nyumba yamapiko. Kenako ndinaona mbalame ziwiri
zikubwera n'kulowa kudzera pawindo. Koma sizimaoneka ngati
mbalame. Anali mwamuna ndi mkazi ndipo onse anali osavala .
. . Kenako ndinaona Guthera ndi Matigari ndipo onse amatuluka
magazi paliponse."
Guthera anachita matha.
"Kunjaku kwada," anatero Guthera. "Kodi dzuwa lalowa kale
kani? Kodi mwaona wapolisi aliyense ngati?"
241