Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 241

Matigari Gawo 16 Pamene Matigari ankafika kumudzi wa ana uja, Muriuki anali atawafotokozera kale anzake aja zonse kupatulapo za mfuti zija. Choncho anawo sanawombe m'manja kapena kukuwa mosangalala, kapena kulumphalumpha ndi chisangalalo, chifu- kwa ankaopa kuti anthu ena adabwapo kenakake akamva kuku- wako. Koma ngakhale anayesetsa kuti anthu ena asadziwe, sa- kanatha kubisa chimwemwe komanso kusirira komwe anali nako pa Matigari. Matigari anapita n'kukalowa m'galimoto ina ya Peugeot. Guthera anakalowa m'chiphapha cha Ford, ndipo Muriuki anap- ita n’kukalowa mu Mercedes-Benz yake. Onse anali atatheratu. Kuyenda komanso kutentha komwe kunali tsikuli kunali kuta- wayamwa mphamvu. Posakhalitsa onse anagona tulo. Ana aja ankalondera. Ena anaima m'malo osiyanasiyana m'mbali mwansewu, ndipo ena anali kumashopu komanso ena anali m'malo ogulitsira zakudya. Anagwirizana kuti ena akangoona apolisi athamange n'kukadziwitsa anzawo, kapena aimbe likhweru lomwe chinali chizindikiro chimene anapatsana. Ena omwe anatsala kumudzi uja ankayenera kuunjika milu yamiyala. Miyala imeneyi akanaswa nayo mitu ya apolisi omwe akanabwera kumudzi wawowo. Iwo anachita zimenezi kuti ate- teze anthu atatu ankagona aja. Anakonzekera kumenya nkhondo. Ena anapanga malegeni komanso magulaye ogendera. Ena anatsegula wailesi ija n'kuyamba kumvera nyimbo. Pam- buyo pa nyimbozo panaikidwa pulogalamu yamapemphero. Amene ankatsogolera patsikuli anali wansembe wina wa ku America wa tchalitchi cha Yesu ndi Mpulumutsi. Pulogalamuyi itatha, kunabwera nkhani. 240