Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 240

Matigari "Yesu adzakupezani muli m'tulotu . . . akamadzabwera." "Ngati mulibe nkhani yoti mundiuze ingokhalani, mu- sayambe kundilalikira za Yesu ine ayi." "Kodi mumamudziwa mkazi wanduna ija? Nduna Yoona Zachilungamo ija? Iye limodzi ndi womuyendetsa anaukiridwa ndi zigawenga moti zawabera galimoto." "Zoona?" "Ndamva zoti amapita kumpikisano wamahatchi . . . kuti akaone mmene hatchi yomwe anagula mogwirizana ndi Aga Khan ikathamangire . . . " "Kodi nawonso anthu akuda ayamba kumagula mahatchi a mpikisano?" "Maendeleo ya muafirika, maedeleo ya wanawake . . . *" Komanso pali zina. Zikumveka kuti akubawo ananyamula zida osati masewera. Anamangirira zida ndi m’mano momwe! *Maendeleo ya muafirika, maedeleo ya wanawake (Kiswahili): Kutanthauza kuti " Amuna a mu africa akamatukuka, azimayinso amatukuka." Matigari ankafuna kuseka moti anavutika kwambiri kuti adziletse. Kenako anawoloka nsewu. "Ingodikirani mdima ugwe. Ndikatenga AK47 yanga pomwe ndinaikwirira," Matigari anadziuza mumtima, "Ndipo ndikabwerako palibe atandifunenso!" 239