Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 24

Matigari Gawo 6 Mwana ankamenyedwa uja ankaopabe mnzake anamumenya uja. Iye ankayenda pang’onopang’ono chakumbuyo kwenikweni kwa gulu la anzakewo. Kenako bambo uja anamupeza. Mwanayo sanazindikire kuti bamboyo akubwera m’mbuyo mwake mpaka pamene anamupeza. Atangozindikira kuti pambali pake pali munthu, anadzidzimuka. “Usaope, ndataya ndodo ija.” Bamboyo anatero. Bamboyo ndi mwanayo anayenda kwa kanthawi asakuyankhulana. Zovala za mwanayo zinali zigamba zokhazokha ndipo nsapato yomwe anavala inkamwetulira moti zala zake zinkaonekera zikusuzumira. “N’chifukwa chiyani mukutilondola?” mwanayo anafunsa bamboyo motero. “Kodi nanunso mukufuna kutibera zinthu zimene tatolazi? Komatu zinthu zimenezi ndi zathu, ndipo ndi phindu limene tapeza, mukudziwa?” “Phindu?” bamboyo anafunsa motero posamvetsa kuti mwanayo akutanthauza chiyani. “Inde, limeneli ndi phindu limene timapeza, zinthu zomwe timatola kumtaya kuja,” mwanayo anatero akumuonetsa zingwe zomwe mnzake uja ankafuna kumulanda. “Kodi anthu ena amakuberaninso zimene mumatolazi?” “Inde amatibera! Akaona kuti tatola zinthu zabwino monga nsapato, malamba komanso zikopa, amabwera akutikukutira mano n’kumatiuza kuti: ‘Kodi zinthu zimenezi mwazitenga kuti, ana akuba inu?’” “Ndi ndani amachita zimenezowo?” 23