Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 239
Matigari
chimene ena akuchifunafuna, njira yabwino ndi kukachibisa pa-
fupi ndi mphuno ya amene akuchifunafunayo." Matigari anatero
mumtima mwake.
Kenako anakumbukira za malo omwetsera mafuta a Esso
omwe anawaona m'mawa wa tsikuli, malowa anali pafupi ndi
Sheraton Hotel, ndipo anawongolera galimotoyo molunjika kumeneko.
Magalimoto onse omwe anaimikidwa kumeneko anali a
Mercedes-Benz okhaokha. Matigari anapeza malo pakati pa
magalimoto enaake ndipo anailowetsa galimotoyo pamenepo.
Kenako anatsegula chitseko cha buti yagalimotoyo n'kukayika
zovala, nsapato komanso kachikwama kam'manja kaja. Kenako
anamenyetsa chitseko n'kuika makiyi m'thumba.
Kenako anayamba kulowera kumene kunali fakitale kuja.
Pamene anafika pamalo omwe anakumana koyamba ndi Nga-
ruro wa Kiriro, Matigari anaima kaye n'kuvula chisoti chake
ndipo anaima pomwepo kwa mphindi imodzi kapena ziwiri.
Asanatulukire munsewu, anamva anthu awiri akukambira-
na. Anthuwa ankakambirana mokhala ngati akufuna kuti iyeyo
amve nawo.
"Kodi munamvera nkhani?"
"Nkhani yake iti? Nkhani yake yonena kuti mtsogoleri wa
dziko lino anayendera masukulu kapena ina, kapena yakuti
walandira chithandizo kuchokera kumaiko ena, kapena yonena
kuti wachenjeza anthu zamphekesera yomwe yafalayi, kapena
yoti wayendera malo ena ija? Nkhanitu pawailesi ndi za apu-
lezidenti, apulezidenti basi! ‘Ee, apulezidenti anali kwakuti, ee
anali kwakuti!’ Apulezidentitu adya wani, akungopezeka kuli-
konse! Ine nkhani zimenezi zanditopetsa! Moti ndangoganiza
zosiya kumvetsera wailesi."
238