Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 238

Matigari Kenako anafika kubwalo losewerera gofu. Kubwaloli kunali kapinga wooneka ngati alibe malekezero ndipo mapaipi ankafaira madzi m'kapingayo. Zinkangokhala ngati mapaipi- wo akuseka monyodola dzuwa lotentha lomwe linali tsikulo. "Kodi m'dziko muno mutadutsa chinkukuluzi, anthu anga- dye khofi, tiyi komanso kapingayu?" Guthera anafunsa mokhumudwa kwambiri. "Tatsala pang'ono kufika!" Matigaria anatero. "Bwalo losewerera gofuli linalipo m'thawi ya Mtsamunda Williams ndi wantchito wake John Boy." "Ndipo lidakalipo masiku ano a Robert Williams ndi John Boy Junior," Guthera anavomereza. "Imikani manja m'mwamba!" anakuwa Muriuki. Iye ankalo- ta akuwopseza munthu ndi mfuti. "Tikufunika tipeze njira yomwe tingakafikire kumudzi wa ana aja kuti ena asatione," anatero Matigari. "Tiyenera kupita m'modzim'modzi kuti asatikayikire," Guthera anapereka maganizo ake. "Ine nditsike panopa, tiku- mana posachedwapa." Guthera anatsikira pakati pa geti lafakitale komanso nsewu wolowera kumsika uja. Muriuki ndi Matigari anapitirira pagalimoto. Muriuki anadzidzimuka ndipo nayenso anatsika n’kusiyana nawo moyo wofewa wa m'galimoto muja. Anakhala ngati walandiridwanso ndi moyo wovuta womwe unali kunja kwa galimotoyo. Kenako Matigari anayendetsa yekhayekha, n'kumasakasaka malo oti aimike galimotoyo. "Ukamafuna kubisa chinthu 237