Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 237
Matigari
"Amangokhaliranso kukamba zamtsogoleri wadziko lino."
Muriuki anawonjezera. "Ingodikirani muone!" Koma kwa kan-
thawi, wailesi ija sinanene zamtsogoleri wadzikolo, Pulezidenti
Ole. Guthera anayamba kumuseka Muriuki.
. . . Zigawenga zoukira boma ku El Salvador zaphulitsa mlatho
womwe uli kulikulu la dzikoli ndi bomba. Zigawengazi zanena kuti
sizisiya kuchita zamtopolazi mpaka boma la USA komanso antchito
awo achikuda a ku El Salvador atavomereza kuti m'dzikomo muchitike
chisankho . . . Tsopano mvetserani nkhani zakwathu konkuno: Mtsogo-
leri wathu wa dziko lino, Pulezidenti Ole . . .
"Ndinakuuzatu ine! Ndinanena ine!" Muriuki anakuwa mot-
ero akusangalala ngati waponda mu ufa, ulosi umene ananena
utakwaniritsidwa. Guthera ndi Muriuki anayamba kuseka
koopsa. Koma sanaseke kwa nthawi yaitali.
. . . Monga mmene munamvera posachedwapa, wamisala m'modzi,
Ngaruro wa Kiriro wamwalira kuchipatala china atawomberedwa . . .
Ngaruro anawomberedwa ndi apolisi ataopseza kuti ayambitsa zachi-
wawa—
"Ayi inuu!" Guthera anatero mwachisoni.
Aliyense anangokhala chete.
Kenako anadutsa mafamu a khofi, tiyi, gonje komanso zi-
nanazi. Ndiyeno anadutsa timinda tina toguga tomwe tinkachi-
ta kuoneka kuti tatoperatu ndi kugwira ntchito.
Pamenepa mpamene Matigari anayankhula.
"Padzikolidi pali magulu awiri a anthu omwe ndi osiyana
kwambiri," ananena zimenezi mokhala ngati akubwereza mawu
a Guthera aja. "Pali anthu omwe amamenyera ufulu wadziko
lawo komanso ena omwe amaugulitsa motchipa."
236