Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 235
Matigari
amene akumayambitsa mavuto m'mabanjamu komanso ku-
chititsa kuti mabanja ambiri aphwasuke. Nanga taonani zimene
wachitazi—kusiyidwa ali mbulanda m’chipululu ngati mmene
muja! Komatu sadula phazi kutchalitchi! Amakonda kupita
kukachita mwambo woyatsa makandulo . . ."
"Dzikoli lazondokadi," Matigari anatero. "Wakuba akumatch-
ula woberedwa kuti wak uba. Wokupha munthu akumatchula
wophedwa kuti wak upha, ndipo munthu woipa akumatchula
wabwino kuti w o ipa. Munthu amene akuyesetsa kuthetsa zoipa
akumaimbidwa mlandu woyambitsa zoipa. Munthu wofunafu-
na choonadi ndi chilungamo akumakathera kundende komanso
kuchipatala cha amisala. Anthu omwe akudzala mbewu
zabwino akuimbidwa mlandu kuti adzala nansongole. Anthu
amene amagulitsa dziko lawo atanganidwa ndi kutsekera
m’ndende anthu omenyera ufulu wadziko lathu. Ena anawatha-
mangitsa m'dziko muno n'kumalola kuti anthu a m'mayiko
akunja azikhala mwaufulu komanso kumakhala moyo
wawofuwofu kwathu kuno. Amene tawasiya kutchire aja si
okhawo amene akuchita zoipa. Ena omwe amayenda m’makwal-
alamu atavala masuti odula amakhala kuti machimo awo
aunjikana mpaka kumwamba, kungoti sagwidwa! Ndithu,
dzikoli lasokonekereratu. Anthu amene amakonda dzikoli
ayeneradi kuchitapo kathu kuti zinthu zisinthe!"
"Komano akabwerera kunyumba mwamuna wake akamuuza
chiyani?" Guthera anafunsa, akuganizirabe mzimayi uja. Koma
palibe anamuyankha.
Matigari anazunguliza chiwongolero ndipo palibe amene
ankayankhula. Aliyense ankangoganizira zake. Nthawi zonse
Muriuki akatseka maso ake, ankaona chi Mercedes-Benz chom-
we ankakhalamo chija chikusintha n'kusanduka chigalimoto
234