Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 234

Matigari Kenaka anayang'ana mitengo, yomwe inkaoneka ngati iku- thamanga n'kumalowera kumbuyo kwa galimotoyo. Guthera ankaoneka kuti ali ndi maganizo aakulu. Nkhope ya mzimayi uja inkabwerabe m'mutu mwake. Kenako anatenga zovala zinali kumbuyo zija n'kuyamba kuziyang'ana mosirira, makamaka diresi ya mzimayi uja. Zovalazo zinali zodula kwa- basi, mwinanso kuposa malipiro omwe antchito ena amapeza akagwira ntchito kwa chaka chathunthu. Kenako anatsegula ka- chikwama kam'manja, ndipo chinachake chinagwera pansi. Chi- nali chithunzi. "Ndinanena ine kuti ndikumudziwa mzimayiyu!" Anatero Guthera. "Ndi ndani?" Muriuki anafunsa. "Chithunzi ichichi ndi chake!" "Cha ndani?" "Mzimayi anali mgalimoto muno uja. Ndi mkazi wa Nduna Yoona Zachilungamo." "Wadziwa bwanji?" "Sasowa m’manyuzipepalamu komanso nthawi zonse amaoneka pa TV. Sabata simatha asanalembe za iye. Ndi ndani amene angalephere kumuzindikira mayi ameneyu? Ndakhala ndikumumva pawailesi akunena zokhudza udindo wa azimayi. Amayankhula osati pang'ono! Amapereka malangizo kwa azi- mayi kudzera pawailesi owathandiza kuti azichita zolongosoka m’mabanja mwawo. Amati, Mzim ayi nd i m unthu w o funik a kwambiri pakhomo. Mawu amenewa sachoka pakamwa pake. Ulendo wina ananena kuti azimayi onse ogulitsa mowa komanso ma- hule onse ayenera kukatsekeredwa kundende chifukwa ndi 233