Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 233
Matigari
Nyumba ankazidutsazo zinali zazikulu molapitsa, komanso
zinali ndi mabwalo aakulu a maluwa. Panja pake panali kapinga
komanso mitengo yobiriwira bwino. M'malo olowera
m'nyumbazi munali mageti akuluakulu azitsulo. Munthu aka-
madutsa munsewu ankatha kuona madamu osambirira odzadza
ndi madzi abuluu. Ngakhale kuti m'dzikomu munali chilala,
nyumbazi zinali ndi madzi okwanira kuthirira kapinga komanso
maluwa. Zinalinso ndi madzi okwanira kudzadzitsa madamu
akuluakuluwo. Pageti iliyonse panali mlonda ndipo pambali
pake panali galu wamkulu. M’mipandayi munalinso zikwang-
wani zolembedwa kuti: "Mbwa Kali."
*Mbwa Kali (Kiswahili): Kutanthauza " Chenjerani. Kuli agalu olusa."
"Kumene tabwera kuno kukungokhala ngati dziko linatu!
Ngati si kwathu komwekunotu." Guthera anatero, ndipo zimene
ananenazi anangokhala ngati waimba ng'oma yowambawamba
chifukwa ndi zimenenso Muriuki ankafunanso kunena.
Msewu umene ankayendawo unalibe mabampu. Nthawi ndi
nthawi ankafika pamalo ochitira chipikisheni ndipo aka-
mayandikira, apolisi ankangowabayibitsa kwinaku akutsegula
chotchingira nsewuwo kuti Mercedes-Benz'yo idutse bwinob-
wino popanda kuchepetsa liwiro.
Muriuki ankalakalaka atatsegula windo n'kuyang'ana
apolisiwo. Iye ankafuna atawauza kuti, "Ndifeyotu amene
mukuwafunafuna aja!" kapena kuwauza kuti, "Uyu ndi Matigari
ma Njiruungi." Iye ankalakalaka ataona zimene apolisiwo
akanachita atazindikira zimenezi.
"Galimotoyi ikungokhala ngati tikiti yolowera kumwamba
ndithu!" Muriuki anatero mosangalala.
232