Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 232

Matigari "Inde ndinabwerapo, kambirimbiri." "Ine kano n'koyamba," anatero Muriuki. Atafika kudera lomwe kunali makampani, Guthera anati: "Kano ndi koyamba kufika mbali ino ya tauni." Anapitirizabe kuyang'ana panja kudzera pawindo, ndipo ankawerenga mayina a zikwangwani zomwe zinali m'mbali mwa nsewu. "General Motors . . . Firestone . . . Coca-Cola . . . IBM . . . Un- iliver Products . . . Madhvani Products . . . Del Monte . . . BAT . . . Union Carbide . . . Mitsubishi Products . . . African Cycle Mart . . ." Kenako anatopa n'kuwerenga zikwangwanizo ndipo anayamba kuganizira za mzimayi uja. Ankadzifunsa kuti, ‘Kodi mayi amene uja ndinamuona kuti?’ Kenako anadutsa nyumba zina za ogwira ntchito. Nyumba zimenezi zinali zazing'ono kwambiri ngati zimbudzi moti ukamazionera patali zinkangooneka ngati zinyalala. Zinali zovuta kukhulupirira kuti munthu wabanja lake angakhale m’kanyumba kakang’ono ngati kameneko. Kenako anayamba kudutsa mafamu. Mipanda yomwe inazungulira mafamuwa in- ali yooneka kuti inamangidwa kale kwambiri moti inali yakuda bii. Ndipo kumpanda kwake kunkaoneka kuti kunalibe chomera ngakhale chimodzi. Anthu oyenda pansi, mabasi, gal- imoto zing'onozing'ono, anjinga komanso ngolo zingapo zinka- kanganirana kuyenda munsewuwo. Kenako anafika kudera limene kunkakhala olemera ndipo Muriuki anayamba kuganiza kuti nyumba zimene ankaona ku- meneku ndi zomwe anaziona m'magazini ya Natio nal Geo - graphic yomwe anaitola m' bini ina. Anang' amba zithunzi za nyumba- zo n'kuzimata m'nyumba yake ija ya Mercedes-Benz. 231