Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Seite 231

Matigari "Ndadziwa zochita tsopano!" Muriuki anatero. "Tiyeni tin- gopita kukaba ndege imodzi kuti tikwere n'kupita kumene kuli mtengo wakacherewo basi." Guthera anaseka. Kenako anafika m'tauni yaikulu yomwe ndi likulu la dzikoli. Pamene ankalowa m’tauniyi, anatulukira munsewu waukulu kwambiri. "Kalekalelo, nsewu umenewu unkatchulidwa ndi dzina la gavanala wina. Gavanala wake anali wachizungu." Guthera anauza Muriuki. "Koma pano umadziwika ndi dzina la Pulezidenti Ole. Misewu yonse yomwe inali ndi mayina a magavanala, mafumu kapena mfumukazi za m'mayiko a at- samunda inasinthidwa mayina moti pano yonse imadziwika ndi dzina la Pulezidenti Ole." "Pajatu nayenso ndi mtsogoleri wathu," anatero Muriuki. Ke- nako patapita kanthawi anafunsa kuti: "N'chifukwa chiyani Pulezidenti Ole samatchulidwa kuti Mfumu, kapena kuti Mfu- mu Pulezidenti!" "Kaya sindikudziwa." Pa nthawiyi m’mbali zonse za nsewuwo munali nyumba zogunda kumwamba. Nyumbazo zinali ndi zikwangwani za- magetsi ndipo zina zinalembedwa kuti: American Express, Citi- bank, Barclays, Bank of Japan, American Life, Inter-Continental, The Hilton, Woolworths, Wimpy Bar, Kentucky Fried Chicken, McDonalds, Shah's Supermarket Stores, Bata Shoes, African Re- tailers komanso ena ambiri. Zikwangwanizo zinkakhala ngati zikukanganirana maso a anthu kuti aziyang'ane. "Kodi unayamba wabwerapo kuno?" Muriuki anafunsa Guthera. 230