Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 230

Matigari "Taonani! Mahatchi! Mahatchi!" anakuwa motero Muriuki. "Mahatchi amenewo ndi amene amachitira mipikisano," Guthera anamuuza choncho. "Kodi ndi kumene anthu a magalimoto onsewa akupita?" "Inde." Khomo lolowera kubwalo lochitira masewerawo linali m'm- bali mwa nsewu. Panali chikwangwani cholembedwa mawu akuluakulu akuti, “CITY JOCKEY CLUB. NDI YOTSEGULA KWA ANTHU A MITUNDU YONSE.” "Kumapita anthu akuda komanso azungu?" "Inde." Iwo anadutsa mpanda wabwalo la maseweralo ndipo mbali inayi kunali bwalo landege. Moyang'anizana ndi malowa kunali chinyumba chachikulu chosungiramo ndege. "Ndege! Ndege! Taonani ndege zing'onozing'ono izo!" Muri- uki anakuwa. "Zimenezi ndi ndege za anthu odzaona malo komanso a ma- bizinezi," Guthera anamuuza choncho. "Anthu olemera ochokera ku America komanso ku Ulaya amabwera kud- zabwereka ndege zimenezi." "Nanga bwanji ndege zikuluzikulu? Bwanji sindikuziona?" "Zimenezo zili kubwalo lalikulu la ndege." "Kodi nawonso anthu akuda amatha kubwereka ndege zime- nezi?" "Ee, ena amabwera kudzabwereka! Anthu monga Boy. Mun- thutu amangofunika kukhala ndi ndalama ngati akufuna kubwereka ndege." 229