Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 229

Matigari m'maganizo mwake. Mercedes-Benz anakwarayo inali yakatukatu. Inali ndi makina oziziritsa mpweya. Inalinso ndi magalasi otsitsa kapena kukweza pogwiritsa ntchito batani. Inalinso ndi makatani m'mawindo akumbuyo. Kumbuyo kwa galimotoyo kunali kabatani kena. Muriuki atakaona anakatobwanya ndipo m'galimotomo munayaka magetsi. Atangochita zimenezi kachitseko kena kanatseguka ndipo mkati mwakemo munali mabotolo a mowa monga Chivas Regal, Gordon's Dry Gin, Bristol Cream Sherry, Green Char- treuse ndi Dom Perignon, komanso munali zakumwa zoziziritsa kukhosi monga madzi a soda, Ginger Ale komanso Coca-Cola. "Koma ndiye ikungokhala ngati nyumbatu!" Guthera anatero. "Zoona galimoto yokhala ndi malo oika mowa komanso zakumwa zosiyanasiyana! Mulinso wailesi yoika matepi." Posakhalitsa Muriuki anatsegula botolo la Coca-Cola ndi mano ake. Kenako anakhala motakasuka pampando wake n'kuyamba kutsopa chakumwacho mwapang'onopang'ono. "Kodi kamphepo kayeziyezika kakuchokera kuti?" anafunsa Muriuki. "Kakuchokera mufani. Galimotoyitu ili ndi makina oziziritsa mpweya," anatero Guthera kuuza Muriuki. Galimotoyo inagwira nsewu waphula ndipo anandondola koopsa. Sinkamveka mabampu ngakhale kuti nsewu wakeyo unali wamayenje. Inkayamwiratu mabampu onse. Muriuki sankakhazikika. Ankangoti wagwira ichi, wagwira ichi. Kenako ankasiya n'kuyamba kuyang'ana pawindo n'ku- maona anthu komanso magalimoto omwe ankadutsa mun- sewuwo. 228