Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 228

Matigari Gawo 15 Mwamuna ndi mkazi anali m'galimoto ija anali mbulanda kumbuyo kwa galimotoyo. Makiyi a galimotoyo anali adakali pachimake. Iwo sankaganiza n'komwe kuti munthu wina anga- fune kuwagwiritsa ntchito m'chipululu ngati mmenemo. Anka- ona kuti palibe amene angafune kubwereka galimotoyo kuthen- go ngati kumeneku . . . Matigari anawasiyira makabudula ankati okha n'kunena kuti, "Ngati mutafalitsa nkhani yoti ndakuberani galimoto lisanafike mawa, ndikaimika galimotoyi m'mbali mwa nsewu n'kuyamba kuonetsa anthu zovala zanuzi kuti aliyense adziwe zimene mumachita kutchire kuno. Koma ngati mukulonjeza kuti simuuza aliyense, ndikaimika galimotoyi pamalo abwino ndipo ndikaotcha zovala zanuzi n'kuwononga umboni wa zimene mu- machitazi. Koma chosankha ndi chanu pamenepa! Ine sindi- vutikayi. Mukambirana kuti mutani awirinu. Ndiye muona ngati mukufuna kuti nkhaniyi ikhalebe yachinsinsi kapena ndiiphed- ule kudziko lonse." Guthera ndi Muriuki anakhala neng’a pampando wa- kumbuyo. Matigali ndi amene anali pachiwongolero. "Kukhala ngati ndinamuonapo mzimayi uja," anatero Guthe- ra atangoyenda kamtunda pang'ono. "Nkhope zina zimakukumbutsa nkhope zinanso. Anthufetu timabadwa awiriawiri!" Matigari anatero motsindika. "Nkhope za anthu ena zimaoneka mofanana. Pajatu tonse tinachokera kwa makolo ofanana. Kungoti chifukwa cha nthawi anthu anabalal- ikira mbali zosiyanasiyana n’kuyamba kuponyana miyala." Guthera anakhalabe chete. Ankaoneka kuti sanakhutire ndi zimene Matigari ananena. Nkhope ya mayi uja inkabwerabe 227