Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 226
Matigari
ulemu kumene anasonyezako. Dzulodzuloli amandifunsa kuti:
‘Kodi tingachite chiyani kuti tithandize Matigari?’ Ambiri mwa
anawo ayamba kale kumadzitchula kuti ndi a Matigari ma
Njiruungi. Amaganizanso zoti atenge zinazake n'kupita nazo
kuchipatala cha amisala kuti akathandize Matigari kuthawa."
"Kodi nzeru imene unapereka ija inali yochokera kwa anza-
kowo? Guthera anafunsa Muriuki. "Koma ana inu ndi anzeru
bwanji! Inudi ndi anthu omenyera ufulu wawo omwe anapu-
lumuka pankhondo yomenyera ufulu," Guthera ananena cha-
pansipansi.
Matigari ankayang'ana kumwamba. Ankaoneka ngati
sankamvetsera zimene enawo ankakambirana.
"Komatu limenelo ndi ganizo labwino!" anatero mwadzidzi-
dzi.
"Mukutanthauza kuti tipite kumudzi wa ana uja? Kapena
mukufuna tikafufuze basi kapena m atatu?" Guthera anamufun-
sa Matigari.
"Ngati titakwera basi kapena m atatu, kapena kupita ku-
mudzi wa ana uja, tikhala tikubisala pamphuno pawo penipeni.
Munthu samagwidwa akamabisala pamalo oonekera. Anthu am-
biri samaona zinthu zomwe zili patsogolo pa mphuno yawo.
Amazisiya n’kumakazifunafuna m’malo obisika!"
"Komatu mabasi komanso m atatu akumachitidwa chipik-
isheni," anatero Guthera.
"Musadandaule, tipeza m atatu yathu," Matigari anatero
kwinaku akuimirira. "Tiyeni tizipita!"
Guthera ndi Muriuki anatsatira Matigari n'kulowa m'katikati
mwa chigwa chija, molowera kumene kunali Mercedes-Benz ija.
225