Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 225

Matigari mzibambo, mzimayi ndi mnyamata ali limodzi adziwitse apolisi nthawi yomweyo." "Ndiye kuti akutifunafuna, si choncho?" Guthera anafunsa. "Zikuoneka choncho," anatero Matigari, akuoneka kuti akus- wa mutu. Kenako tsinya linaphophokanso pachipumi pake. "Kuti tikafike kumene kuli mtengo wakacherewo tiyenera kudutsa misewu yambiri, ndipo tikumana ndi anthu ambiri. Tikhoza kumangidwa tisanakafike n’komwe." "Tikhozanso kumangidwa tisanakafike kunyumbako," Guthera anawonjezera. "Ndalumbira kuti Boy asagonenso m'nyumba ya ine usiku wina. Komanso ine ndi iyeyo sitingamakhale nyumba imodzi," anatero Matigari, akuoneka kuti akumva ululu ndi mawu ame- ne Guthera ananena aja. "Ndiye titanino?" Guthera anafunsa. "Ngati titapeza basi kapena m atatu, tikhoza kupita kaye ku- mudzi wa ana aja n'kukabisala mpaka dzuwa litalowa. Kenako usiku, tikanyamuka n’kupita kumene kuli mtengo wakachere uja kuti ndikatenge mifuti komanso chikandalanga changa. Tikakachoka kumeneko tikapita kwa Boy ndi Williams n'kukamuuza kuti: Manja m 'm wam ba! Im ik ani m anja m wam ba ngati simukufuna kuti ndipange mibowo yazipolopolo m’mitu mwanu- mo!" "Mukutanthauza kuti anawo akatisunga m'magalimoto awo aja?" Guthera anafunsa akuseka. "Inde! Ndipotu amafunitsitsa atagwirana chanza ndi Matiga- ri. Kungochokera pamene anamugenda paja akhala akufunafu- na njira yoti apepesere kwa Matigari chifukwa cha kupanda 224