Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 224

Matigari Kenako anaona Muriuki akuyandikira Mercedes-Benz ija. Iye anayenda mozungulira galimotoyo n'kuipitirira pang'ono. "Zikutheka bwanji kuti woyendetsa galimoto asatuluke kuti ataye madzi?" Guthera anafunsa. "Ndi ndani amene anakuuza kuti oyendetsa magalimoto akaima amafunika kutaya madzi?" "N'chifukwa chiyani mwayamba poyerayera kuwaikira kum- buyo oyendetsa galimoto? Kodi nanunso munali woyendetsa galimoto?" "Ndani, ineyo? Palibe ntchito yomwe ungaitchule yomwe sindinagwirepo. Ndachita chilichonse chimene ungachiganizire ndipo zonsezi ndinkachitira atsamuda osayamika aja." Kenako anaona Muriuki akubwerera. Atamuona anayamba kumudikira ndipo Muriuki anabwerako akumwetulira mwau- tambwali. "Ndi ndani?" Guthera anafunsa. "Ndi mzimayi ndi mzibambo," Muriuki anatero, akuyesetsa kudzigwira kuti asaseke. "Akuchita chiyani?" Muriuki anayamba kuseka koopsa. Guthera anayang'ana Matigari, yemwe sanasinthe mmene ankaonekera. "Anzanu ali m'chikondi. Achotsa zovala zonse. Ayatsa wailesi, koma akuoneka kuti sakumvetsera wailesiyo." "Asiyeni amenewo. Tiyeni tizipita." Anatero Matigari. "Tiwasiye chifukwa chiyani?" Guthera anafunsa. "Ndamva pawailesi akulengeza kuti apolisi atseka misewu yonse ikuluikulu. Komanso alengeza kuti aliyense amene ataone 223