Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 223
Matigari
Anali wokondwa zedi. "Minyangayotu amagulitsa ndalama
zankhaninkhani. Kodi si paja munanena kuti pali atambwali
ena omwe amagulitsa chimanga chadziko lino kumayiko ena?
Amakhala akusinthanitsa chimangacho ndi makobidi ankha-
ninkhani moti amalemera koopsa. Ndi zimenensotu zimachi-
tika ndi minyanga ya njovu. Amaigulitsa kwa anthu ena adyera
ochokera m'mayiko a amwenye komanso ku Ulaya.
Amawononga zinthu zachilengedwe n’cholinga choti apeze
chilembwe."
"Kodi akapoli amenewa sadziwa kuti zinyama ndi mabwen-
zi a anthu? Pamene tinali kunkhalango sitinkapha nyama
mwachisawawa pokhapokha ngati tili ndi njala kapena ngati
chakudya chatithera. Ndipo nthawi zina tikaona nyama
yovulala, tinkaisamalira poimanga pamene yavulalapo. Nyama
zinali zofunika kwambiri kwa ife. Zinkatichenjeza
kukamabwera zoopsa. Kodi umadziwa kuti anthu amatha
kuyankhula ndi zinyama? Ngati utadzakhala munkhalango
kwa nthawi yaitali nawenso udzaphunzira kuyankhula ndi
zinyama. Nthawi zina nyama imatha kukuyankhula. Umafu-
nika kungokhala chete, n'kuimvetsera. Kodi ukuganiza kuti
abusa aziweto amakwanitsa bwanji kukhala zakazaka m'tchire
muno chinachake osawavulaza? Iwo amakhala anapanga
mgwirizano wapadera ndi zinyama ndipo zinyamazo zim-
awachenjeza kukamabwera zoopsa."
"Anthu omwe amayendetsa magalimoto opuma ngati ame-
newa amakhala kuti akolopola ndalama za ogwira ntchito om-
we akungothimbirira ndi umphawi. Amangowalima anzawo
pamsana basi," anatero Guthera.
222