Agoloso Presents - Atondido Stories Agoloso Presents - Matigari | Page 222

Matigari komanso nkhosazo. Ukaone kuti akuchita chiyani m'galimoto- mo. Koma uchite zinthu mosamala. Paja amati kuchita zinthu mosamala sikusonyeza kuti munthu ndi wamantha. Kenako ukaona zomwe akuchita, ukazungulire uko n'kudzatipeza kuno. Koma uonetsetse kuti amene ali m'galimotowo asakuone ukubwereranso kuno." Muriuki anafufuza ndodo. Kenako anaiika paphewa lake n'kugwira mbali zonse ndi mikono yake monga mmene oweta ng’ombe amachitira. "Kodi unaphunzira kuti kuchita zimenezi? Kodi nawenso unakhalapo m'busa waziweto?" Guthera anafunsa Muriuki kwinaku akuseka. "Ayi, ndikungotengera zimene ndinaona abusa aziweto aku- chita." "Ngati patachitika chinachake chomwe chingachitse kuti ti- sakumanenso," anatero Matigari, "Ungopita kunyumba yathu madzulo ano." Muriuki anawasiya atagona pansi kuti anthu anali m’gal- imoto ija asawaone ndipo chidwi chawo chinali kumene kunali galimoto ija. "Mwinatu ndi anthu ozembetsa minyanga ya njovu," Guthe- ra anatero. "Ndiye angapeze chiyani pozembetsa minyanga ya njovu? Bolatu zikanakhala kuti nyangazo zimadibwa." "Koma ndiye mwakhaladi m’tchire kwa nthawi yaitalitu," Guthera anatero akuseka. Tsiku limeneli zinkaoneka kuti zinkamuyendera Guthera chifukwa ankaoneka kuti sanadzukire kumanzere. 221